NDAKUSOWA . Ndakusowa wokondedwa wanga Zikanakhala kuti ndi zotheka Ndikanatuma mphepoyi kuti idzasiye Uthenga womwe uli mu mtima mwanga Uthenga wa chikondi cha ine kwa iwe . Ndikakhala ndimalingalirabe Malonjezano omwe tinkapatsana Ndikagona ndimalotabe Chikondi chomwe tinkagawana Ndikamayenda ndimalingalilabe Zabwino zomwe tinkachitirana Nthawi zonse mumtimamu Za iwe ndimaganizabe . Ndakusowa wokondedwa wanga Kanjira kaja ndimadutsadutsabe Ndi chiyembekezo kuti mwina tingakumane Malo aja ndimakhalakhalabe Kuti mwina diso lokha ndingakuthileko . Ndi zovuta kukuyiwala Ndikakumbukira nkhope yako yowala Kukongola kwako ukamwetulira Mtimawu zikuvuta kukuyiwala Kulikonse uliko Ine ndakusowa wokondedwa wanga
Next PostNewer Posts Previous PostOlder Posts Home