NDAKATULO -NDAKUSOWA
NDAKUSOWA
.
Ndakusowa wokondedwa wanga
Zikanakhala kuti ndi zotheka
Ndikanatuma mphepoyi kuti idzasiye
Uthenga womwe uli mu mtima mwanga
Uthenga wa chikondi cha ine kwa iwe
.
Ndikakhala ndimalingalirabe
Malonjezano omwe tinkapatsana
Ndikagona ndimalotabe
Chikondi chomwe tinkagawana
Ndikamayenda ndimalingalilabe
Zabwino zomwe tinkachitirana
Nthawi zonse mumtimamu
Za iwe ndimaganizabe
.
Ndakusowa wokondedwa wanga
Kanjira kaja ndimadutsadutsabe
Ndi chiyembekezo kuti mwina tingakumane
Malo aja ndimakhalakhalabe
Kuti mwina diso lokha ndingakuthileko
.
Ndi zovuta kukuyiwala
Ndikakumbukira nkhope yako yowala
Kukongola kwako ukamwetulira
Mtimawu zikuvuta kukuyiwala
Kulikonse uliko
Ine ndakusowa wokondedwa wanga
0 comments:
Post a Comment