NTCHENTCHE ZOULUKA ZIVUTA KU LILONGWE
Tsiku limenelo tidakhala pa Wenela ndipo Abiti Patuma adati tipite ku Lilongwe kumenetu ndalama zabooka malinga ndi ungano wa aphungu komanso malonda a fodya.
Adati nditsagane nawo kumeneko.
Tidaimatu pa Roundabout pa Kameza kuimitsa galimoto iyi ndi iyo. Nthawiyo nkuti Abiti Patuma atapita kukagula madzi koma atangobwera, galimoto zitatu zidatiimira.
“Anti, mukupita kwa Chingeni? Tiyeni,” adatero mkulu mmodzi.
“Ayi ndithu,” adayankha Abiti Patuma.
art
“Inetu wa ku Mwanza, mukupita kumeneko? Kwerani ulere anthu atatu, mzimayiyo akhale kutsogolo,” adateronso mkulu wina wa galimoto yake yopuma.
Abiti Patuma adapukusa mutu. Ndidagwira m’chiuno, kuthodwa.
Posakhalitsa padatulukira galimoto ina yofiira. Sindinaonepo galimoto yopuma ngati imeneyo.
“Tikukakhazikitsa galimotoyi ku Lilongwe. Ya madzi iyi. Mtidzi osanena. Tiyeni,” adatero amene amayendetsayo.
Ndani akadakana mayesero okwera galimotoyo? Abiti Patuma adakwera kutsogolo.
Nkhani imodziimodzi zidali kuphulika.
“Ndikuchokera ku Nansadi ku Thyolo. Ndaona kuti kukumangidwa nyumba zina. Mudzi uja basi ukhala tauni, Blantyre kulenga,” adatero mkuluyo, tikudutsa pa Zalewa.
Apolisi adali mbweee! Koma palibe adaimika galimotoyo.
“Mwati ku Thyolo kukumangidwa nyumba zina?” adafunsa Abiti Patuma.
“Sindinatero. Malo angopezeka kuti pamangidwenso manor ina. Mulimba?” adafunsa mkuluyo.
Abale anzanga, musandifunse kuti amatanthauzanji chifukwa sindikuyankhani. Nanga kwathu kwa Kanduku ziliko izi za ma manor?
“Mpumulo wa Noma nawo ulipo kale. Kodi simukudziwa iyi ndi penshoni? Ndani safuna zabwino kuukalamba?” adafunsa mkulu uja.
Adandipindanso.
Tsono titafika ku Lilongwe, mkulu uja adati tizungulire.
Ndisaname, tidazungulira monse adayenda anyamata aja asadaomberane kalelo. Mukuwadziwa. Aja adazungulira Lilongwe yonse akusakana, mikangano ya ziboliboli kufuna kusinthitsa ndalama… kuzungulira malo onse omwera mpaka kukaomberana pachipata kulimbirana ndalama zobooka za Adona Hilida.
Koma Adona Hilida ali kuti? Kodi nsalu ija ankapachikira paphewa akupachikabe? Nanga Richie, bambo wa kwawo akupita nawo konse ayenda muja ankachitira kalelo?
Tidafika ku Nyumba ya Malamulo. Tidapeza anthu akupha tulo. Inde, adali atalumidwa ndi kashembe, ntchentchefly ija yotchedwa tsetse imene imayambitsa trypanosomiasis, nthenda yogonetsa.
“Tsono mkulu akupha tulo apayu, uyu Joliji, mwati akudzatenga fupa la Moya Pete? Nanga tulo take timeneti adzatithandiza?” adanong’ona Abiti Patuma.
“Mwamuiwala kodi? Pajatu ankati aletsa zotsitsa mpweya pagulu,” ndidatero.
“Tsono momwe mukumuonera iyeyo, akuchita emit ma gas ochuluka bwanji to bring environmental degradation or is it climate change?” adafunsa Abiti Patuma.
Adandipinda.
“Sindimagona ine. Ndimaphethira ine. Ine wanuwanu, amene ndidzatenge mpando wa Moya Pete sindimagona ine. Ndimaphethira ine. Mwana wanga ndi msangalatsi…. mwamuiwala Izeki? Mwana wanga ankafuna kukhala ngati Izeki. Koma ineyo ndikufuna kudzakhala Moya Pete, musandiipitsire mbiri ndi za tulo,” adalira munthu wamkulu.
Abiti Patuma adamupatsa sand paper. Ati chibwano kaya chatani kaya….
Gwira bango iwe! Upita ndi madzi!!!