Kumadera Okwera
Kumadera Okwera
Unduna woona za ulimi wa mthirira ndi chitukuko cha madzi wapempha anthu omwe akukhala m`madera otsika m`boma la Karonga kuti asamukire kumadera okwera.
Unduna wu wanena izi kudzera m`chikalata chomwe watulutsa potsatira lipoti lomwe nthambi ya zanyengo latulutsa report lomwe likuti m`bomali mugwa mvula yambiri kwa masiku asanu akudzawa yomwe ikhonza kuchitisa madzi osefukira.
Kudzera m`chikalatachi chomwe chasayinidwa ndi mkulu woona za ulimi wa nthirila ndi chitukuko cha madzi, a Sandram Maweru, mvulayi ichititsa kuti mitsinje ya Songwe, North Rukuru komanso Lufilya isefukire zomwe ati zikhoza kuononga katundu komanso anthu kutaya miyoyo.
M`chigawo chakumpoto mwagwa mvula yambiri yomwe yachititsa anthu ena kutaya miyoyo yawo komanso kusowa pokhala.
0 comments:
Post a Comment