M'BUSA AGWIDWA KAMBA KOGWILIRA MZIMAYI WA MISALA
M'BUSA AGWIDWA KAMBA KOGWILIRA MZIMAYI WA MISALA
Apolisi ku Dowa amanga m`busa wina yemwe ndi mzika ya dziko la Democratic Republic of Congo wa kumalo osungirako anthu othawa kwawo a Dzaleka m’bomalo kamba komuganizira kuti adagwirila mzimayi wamisala.
Ofalitsa nkhani za apolisi ku Dowa Constable Godfrey Kaponda atsimikiza za nkhaniyi ndipo ati m’busayo Emanuel Bachenezi wa zaka 28 wa Mpingo wa Integrity Family Church ku Dzaleka komweko, ndipo
amachokera m`dera la Bukavu m`dziko la Democratic Republic of Congo (DRC).
Iye akumuganizira kuti anagwilira mzimayi wa zaka 26 zakubadwa yemwe amachokeranso dziko la Democratic Republic of Congo m’mwezi wa October chaka chatha,ndipo pano ndi woyembekezera.
“M’busayo anapita ku nyumba kwa mzimayiyu kukamupemphelera kuti achire matenda amisala .
M’busa Bachengezi adanamiza zimayiyu kuti Mulungu wamuonetsa kuti mayiyu amwe mankhwala anayi nthawi imodzi osati amodzi monga momwe adamulangizira ku chipatala”, watero Kaponda.
Izi akuti zidachititsa kuti zimayiyu agone tulo tofa nato ndipo m’busayo adapeza mwayi womugwirila.
“M’busayo adagona kunyumba ya mayiyu ndipo atafunsidwa m’mawa iye adauza mayiyo kuti amamuchotsa ziwanda za mwamuna wake yemwe adamwalira kalekale”,watero mneneli wa a polisiyu.
Poopa kumangidwa m’busayo adanamiza mzimayiyu kuti amukwatira koma patatha masabata angapo
mayiyu adatengera nkhaniyi ku bwalo la First Grade Magistrate.
“Bwaloli linati mlanduwu ndi wa pa chiweniweni ndipo m’busayu amayenera ku kumupepesa
mzimayiyu”,watero Kaponda.
M’busayu akuyembekezeka kukayakha mlandu wogwilirira zomwe zikusemphana ndi gawo 139 la
malamulo oweruzira milandu dziko lino .
0 comments:
Post a Comment