ALANDULIDWA PA BANJA KU BUNDA M;BOMA LA LILONGWE
Mai wina ku Bunda kwa Chadza mboma la Lilongwe manja ali nkhongo atamulandula pa banja.
Nkhaniyi ikuti mayiyo ali pa chiwiri ndi Nyakwawa ina mderalo. Nyakwawao yemwe amagwira ntchito anafika nthawi yoti alandile gradulity ku kampaniyo ndipo anaganiza zopereka ndalama kwa akazi akewo kuti mwina mkuyambira bizinesi. Nyakwawayo inapereka ndalama yofanana koma mkazi wa mng’onoyo ananyinyirika ndikuchepa kwa ndalamayo ponena kuti iye ndi njole kuyekeza ndi mkazi wamkulu yemwe iye amati ndi gogo amene. Pokwiya ndi nkhaniyi Nyakwawayo inasamuka mkukakhala kwa mkazi wa mkuluyo ndipo mkazi wadzimva uja naye anatenga zovala zonse zomwe anasiya nyakwawayo mkukabisa pa chulu. Paja pali mau amati padziko palibe chinsinsi, atamufunsa ndipo iye nkuyankha kuti sakudziwa komwe kunapita zovalazo, anthu ena akufuna kwabwino anauza nyakwawayo za komwe kunali zovalazo. Nyakwayo itapeza zovalazo anakazichapa ku mtsinje koma mozemba pochita manyazi ndi zomwe zinamuchitikirazo ndipo aliyense wokomana nawo amawauza kuti ndanyamula mphonda. Apa nyakwawayo sinachedwetse koma kulandula mayiyo kunena kuti banja latha. Pakadali pano mayiyo manja ali ku nkhongo chifukwa chomulandula pa banja.
ATHAMANGITSIDWA KAAMBA KA UMFITI KU PHALOMBE
Anthu a mudzi wa Mandeule Kwa Kaduya m'boma la Phalombe apitikitsa mkulu wina m’deralo kamba komuganizira kuti ndi mthakathi wotheratu. Nkhaniyi ikuti mkuluyu kwao ndiku Mozambique ndipo inadzapempha malo malo m’deralo zaka zapitazi ndipo zikumveka kuti kuyambira nthawiyo wakhala akuphunzitsa ana a eni uthakati. Nkhaniyi yaulurika pamene m’modzi mwa anawo yemwe ndi wa zaka zisanu ndi zitatu anafotokozera makolo ake zomwe wakhala akuchita mogwirizana ndi mkuluyu. Mwa zina mwanayu anafikanso poulula kuti mkuluyu anamusungitsa mvula ndipo akumuuriza kuti asamayendeyende pofuna kuonetsetsa kuti mvulayo isagwe. Anthu ambiri mderalo akwiya ndi nkhaniyi maka poganizira
ng’amba yomwe yavuta kwambiri kumeneko ndipo zimenezi ndi zomwe zachititsa kuti anthuwa aonetse mthakatiyu msana wa njira.
0 comments:
Post a Comment