HENRY MUSSA A KUSOWA TULO NDI THEBA
HENRY MUSSA AKUSOWA TULO NDI THEBA
Anthu omwe adagwirako ntchito m’migodi ya m’dziko la South Afrika pamgwirizano wa Temporary Employment Bureau of Africa (Teba) kapena kuti ‘Joweni’ akhala akudandaula kwa nthawi yaitali pankhani yokhudza ndalama zawo za penshoni. Sabata zingapo zapitazi nduna ya zantchito Henry Musa idapereka chiyembekezo m’mitima ya anthu odandaulawa powauza kuti boma la Malawi ndi South Africa ali kumapeto kwa zokambirana pankhaniyi kuti anthuwa alandire ndalama zawo Mawlawi daily nkhani adacheza naye motere:
Tadzifotokozeni mwachidule, olemekezeka.
Ine ndine Henry Mussa, phungu wa dera la kummawa kwa boma la Chiladzulu, komanso ndine nduna ya zantchito ndi kuphunzitsa anthu ntchito.
Mussa: Nkhani ya Teba sikutigona nayo
Mussa: Nkhani ya Teba sikutigona nayo
Pali gulu la anthu omwe adapita kukagwira ntchito m’diko la South Afrika pamgwirizano wa Teba omwe mpaka pano akuti sadalandirebe ndalama zawo za penshoni. Inu ngati nduna ya zatchito mukudziwaponji?
N’zoonadi anthu amenewa sadalandire ndalama zawo koma akhulupirire kuti ifeyo sitikugona chifukwa cha nkhani yomweyi. Tili kalikiriki kukambirana ndi dziko la South Afrika kuti anthu amenewa athandizike basi chifukwa ndalamazo ndi zawo osati za munthu wina kapena kuti akupemphetsa, ayi.
Komanso tamva kuti maina ena akusowa m’kaundula kodi pamenepa zikukhala bwanji?
N’zoona pamaina 36 875 omwe adaperekedwa ku South Afrika, maina 9 440 okha ndiwo adapezeka m’makina a kompyuta, kutanthauza kuti maina 23 427 akusowa.
Mainawa akusowa chifukwa chiyani?
Inde, tidafufuza nanga unduna ukulukulu ngati uno ungangokhala chete pankhani yaikulu ngati imeneyi? Pali zifukwa zingapo. Choyamba, anthu ena amalakwitsa maina ndi manambala a pachiphaso polemba, nanga mmesa akhala nthawi yaitali. Chachiwiri, anthu ena panthawiyo amachita chodinda chala kaamba kosatha kulemba koma adamwalira ndiye amasayinira chikalata chawo ndi abale awo, zomwe zidachititsa kuti asakapezeke m’makina kumeneko.
Ndiye ngati unduna, anthu oterowo muwathandiza motani?
Tidakambirana kale ndi dziko la South Afrika kuti aunikenso moti ndikunena pano anthuwo akusayinanso makalata ena kuti titumize ku South Afrika.
Kaperekedwe kake ka ndalamazo kadzakhala kotani?
Choyamba ndinene kuti nkhani ya Tebayi imakhala ngati ikuvutavuta chifukwa chakuti pena pake anthu amaona ngati ndalamazo zidabwera kalekale koma boma likuchitira dala osapereka kwa eni ake. Muwauze anthu kuti ndondomeko yake ndi yoti munthu aliyense adzapereka momwe akufuna kudzalandirira ndalama zake. Omwe ali ndi maakaunti kubanki adzapereka komanso omwe alibe, adzapereka njira yomwe angalandirire ndalamazo ndipo akatenge okha.
0 comments:
Post a Comment