ANA ATATU AFA KUDOWA PA NGOZI ZOSIYANASIYANA
ANA ATATU AFA KUDOWA PA NGOZI ZOSIYANASIYANA
Ana awiri ku Mponela m’boma la Dowa afa chipupa cha nyumba yomwe anagona chitawagwera.
Mneneli wa apolisi ku Mponela a Kondwani Kandiado atsimikiza za nkhaniyi ndipo ati ,anawo ndi Angella Hastings wa zaka zinayi komanso Lonjezo Hastings wa zaka zisanu ndi chimodzi ochokera m’mudzi mwa Chimkuwu mdera la mfumu yayikulu Chakhaza m’bomalo.
Panthawiyo anawo amagona m’nyumbayo usiku wa loweruka lapitali pamodzi ndi makolo awo.
Nyumba yomwe anthuwo adagona akuti imadontha kwambiri kamba ka mvula yamphamvu yomwe imagwa
kuderalo, zomwe zidachititsa kuti khoma lanyumbayo linyowe ndi kugwera banjalo.
“Anawa amagona ndi makolo awo m’nyumba yomwe imadotha kamba ka mvula yambiri yomwe imagwa
deralo, pakati pa usiku anthu anamva mfuwu odabwitsa kunyumbako ndipo anakapeza chipupa cha nyumba chitagwera banjalo. Anthu analitengera banjali ku chipatala koma Angella komanso Lonjezo anali atafa kale ndipo amayi komanso mwana wina anangovulala,” watero Kandiado.
Ku Dowa komweko mwana wa zaka zisanu ndi chimodzi wafa, jeke lodindira fodya litamugwera pantima. Caroline Jonathan adamwalira pa chipatala cha mishoni cha madisi jekeyo atamugwera kuchokera pomwe adamuika . Panthawiyi mwanayo amasewera ndi amzake. Caroline Jonathan amachokera m'mudzi mwa Malenga mfumu yaikulu Chakhaza bomalo.
0 comments:
Post a Comment