Jekete ya mlonda iyankhula 

Jekete ya mlonda iyankhula  Akuluakulu apa sukulu ina yogonela pompo ku Dedza anachita mantha atamva jekete ya mlonda wina ikuvomera pomwe anthu-wo amaitana mlonda-yo. Nkhani-yi ikuti sukulu-yo ili mu mpanda ndipo inalemba mlonda wina yemwe amakhala pa ka nyumba kena komwe kali pa chipata cha mpanda-wo. Tsiku lina mmodzi mwa ophunzira apa sukulu-po anadwala ndipo ataona kuti sapilila anadzutsa akuluakulu ena a sukulu-yo ncholinga choti amupelekeze ku chipatala. Apa anthu-wo akuti anapita pa chipata-po ncholinga choti atuluke ulendo wakuchipatala-ko. Koma anthu-wo anapeza chipata-cho chokhoma ndipo apa mmodzi mwa anthu-wo akuti anayamba kuitana dzina la mlonda-yo pamenepa mkuti ataima panja pa ofesi ya mlonda-yo momwe munali jeteke yokha yomwe anaikoleka pa msomali. Anthu-wo akuti anadzidzimuka mu jetekemo mutachoka mau kuti “MADAME “ kuyankha kuitana-ko. Anthu-wo akuti anaona ngati sanamve bwino komwe mau amachokera. Ndipo pofuna kutsimikiza komwe kumachokera mau-wo mmodzi mwa akuluakulu apa sukulu-po anaitananso ndipo monga poyamba jeketeyo inayankhanso. Apa anthu-wo akuti anachita mantha kwambiri ndipo anatasunthila kutali kuchoka pa chipata cha kanyumba ka mlonda-yo. Mlonda-yo akuti anatulukila mbali ina ya sukulu-yo. Ndipo akuluakulu a sukulu-yo atafunsa mlonda-yo za komwe amachokera pomwe mau ake amamveka mu jekete mlonda-yo akuti anayankha mopanda manyazi koma mwachidule kwambiri kuti ntchito ya ulonda ndi yovuta. Apa akuluakulu a sukulu-yo akuti anangoti kukamwa yasaa kusowa choyankha mlonda-yo.
Next PostNewer Post Previous PostOlder Post Home

0 comments:

Post a Comment