Aphana kamba ka mowa

Aphana kamba ka mowa Mwamuna wina wafa kwa Bvumbwe mboma la Thyolo nzake yemwe amakanganirana naye mowa atamubaya ndi mpeni. Nkhaniyi ikuti amuna awiriwo anatengana kupita pa malo ena omwera mowa ndipo anayamba kuitanitsa umodzi-umodzi. Mowawo utatsala botolo limodzi, amuna awiriwa anayamba kukanganirana ndipo wina popsya mtima anatulutsa mpeni nkumubaya nzakeyo m’mutu ndipa mimba. Anthu ena achifundo anatengera mwamunayo ku chipatala chapa boma ku Thyolo komwe anakamwalira. Apolisi atsimikiza nkhaniyi ndipo ati mwamuna yemwe wapha nzakeyo ndi Kondwani Mwapaleya wa zaka 19 pamene ophedwayo ndi Kenneth Maseya wa zaka 21. Pakadali pano Mwapaleya akumusunga m’chitokosi cha apolisi podikira kukaonekera ku khothi komwe akayankhe mlandu wakupha munthu posachedwapa.    
Next PostNewer Post Previous PostOlder Post Home

0 comments:

Post a Comment